Jeremiah 50:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lupanga lilunjike pa akavalo ake ndi pa magaleta ake, lilunjikenso pa magulu ankhondo achilendo amene ali pakati pao, kuti asanduke ngati akazi. Lupanga lilunjike pa chuma chake chonse, kuti chidzafunkhidwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lupanga lili pa akavalo ao, ndi pa magaleta ao, ndi pa anthu onse osanganizidwa amene ali pakati pake, ndipo adzakhala ngati akazi; lupanga lili pa chuma chake, ndipo chidzalandidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Imfa ilunjike pa akavalo ake ndi magaleta ake. Ilunjikanso pa magulu ankhondo achilendo amene ali pakati pawo kuti asanduke ngati akazi. Chiwonongeko chilunjikenso pa chuma chake kuti chidzafunkhidwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lupanga liri pa akavalo ao, ndi pa magareta ao, ndi pa anthu onse osanganizidwa amene ali pakati pace, ndipo adzakhala ngati akazi; lupanga liri pa cuma cace, ndipo cidzalandidwa.