Jeremiah 50:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chilala chilunjike pa madzi ake, kuti adzaphwe. Paja dzikolo nlamafano, anthu ake achita kuyaluka nawo mafanowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chilala chili pa madzi ake, ndipo adzaphwa; pakuti ndi dziko la mafano osema, ndipo ayaluka ndi kufuna zoopsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chilala chilunjike pa madzi ake kuti aphwe. Babuloni ndi dziko la mafano, ndipo anthu afika poyaluka nawo mafanowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cirala ciri pa madzi ace, ndipo adzaphwa; pakuti ndi dziko la mafano osema, ndipo ayaruka ndi kufuna zoopsa.