Jeremiah 50:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake ku Babiloni nyama zakuthengo zizidzakhalira limodzi ndi afisi, ndipo nthiŵatiŵa zizidzakhalamonso. Tsono kumeneko sikudzakhala anthu mpaka muyaya. Sikudzapezeka munthu ndi mmodzi yemwe pa mibadwo yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake zilombo za kuchipululu ndi mimbulu zidzakhalamo, ndi nthiwatiwa zidzakhala m'menemo; ndipo sadzakhalamo anthu konse; ndipo sadzakhalamo m'mibadwomibadwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nʼchifukwa chake nyama zakuthengo ndi afisi zidzakhala kumeneko ndipo kudzakhalanso akadzidzi. Kumeneko sikudzapezekako anthu, ndithu anthu sadzakhalako pa mibado yonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace zirombo za kucipululu ndi mimbulu zidzakhalamo, ndi nthiwatiwa zidzakhala m'menemo; ndipo sadzakhalamo anthu konse; ndipo sadzakhalamo m'mibadwo mibadwo.