Jeremiah 50:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Onani, ankhondo akubwera kuchokera kumpoto. Anthu a mtundu wanyonga ndi mafumu ambiri akunyamuka kuchokera ku madera akutali a dziko lonse lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, anthu achokera kumpoto; ndiwo mtundu waukulu, ndipo maufumu ambiri adzaukitsidwa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Taonani! Gulu lankhondo likubwera kuchokera kumpoto; mtundu wa anthu amphamvu pamodzi ndi mafumu ambiri, wanyamuka kuchokera kumathero a dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, anthu acokera kumpoto; ndiwo mtundu waukuru, ndipo mafumu ambiri adzaukitsidwa kucokera ku malekezero a dziko lapansi.