Jeremiah 50:42 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atenga mauta ndi mikondo, ngankhalwetu, ndiponso opanda chifundo. Phokoso lao lili ngati mkokomo wa nyanja. Akwera pa akavalo, atavala zankhondo, kuti adzamenyane nawe, iwe mzinda wa Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, ndipo akwera akavalo, yense aguba monga munthu wa kunkhondo, kukamenyana ndi iwe, mwana wamkazi wa Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atenga mauta ndi mikondo; ndi anthu ankhanza ndipo alibe chifundo. Phokoso lawo likumveka ngati mkokomo wa nyanja. Akwera pa akavalo awo, ndipo akonzekera kudzakuthira nkhondo iwe Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe cifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, ndipo akwera akavalo, yense aguba monga munthu wa kunkhondo, kukamenyana ndi iwe, mwana wamkazi wa Babulo.