Jeremiah 50:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya ku Babiloni idamva za mbiri yao, ndipo yachita kuti m'nkhongono zii! Yada nkhaŵa, ikumva kuŵaŵa ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mfumu ya ku Babiloni yamva mbiri yao, ndipo manja ake alefuka; wagwidwa ndi nkhawa, ndi zowawa zonga za mkazi alimkudwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya ku Babuloni yamva za mbiri yawo, ndipo yalobodokeratu. Ikuda nkhawa, ikumva ululu ngati wa mayi pa nthawi yake yochira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mfumu ya ku Babulo yamva mbiri yao, ndipo manja ace alefuka; wagwidwa ndi nkhawa, ndi zowawa zonga za mkazi alimkudwala.