Jeremiah 50:44 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Monga momwe mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yordani umaopsera khola lankhosa lotetezedwa bwino, Inenso mwadzidzidzi ndidzapirikitsira Ababiloni kutali ndi kwao. Pambuyo pake ndidzaŵaikira woŵalamulira amene ndidzamufune Ine. Nanga ndani angafanefane ndi Ine? Ndani angandipititse ku bwalo lamilandu? Ndi mtsogoleri uti amene angalimbike pamaso panga?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, mtundu uja adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzauthamangitsa umchokere, ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake; pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, monga mkango wochokera ku nkhalango ya ku Yorodani kupita ku msipu wobiriwira, momwemonso ine ndidzapirikitsa Babuloni mʼdziko lake mwadzidzidzi. Pambuyo pake ndidzawayikira wowalamulira amene ndamufuna Ine. Wofanana nane ndani ndipo ndani amene angalimbane nane? Ndi mtsogoleri wa dziko uti amene anganditengere ku bwalo la milandu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, mtundu uja adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wocokera ku Yordano wosefuka; koma dzidzidzi ndidzauthamangitsa umcokere, ndipo ali yense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wace; pakuti wakunga Ine ndani? adzandiikira nthawi ndani? ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?