Jeremiah 50:45 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake imvani, zimene Ine Chauta ndakonza zolangira Babiloni, ndiponso zolinga zanga zolangira dziko la Ababiloni ndi izi: Ndithudi, ndi ana omwe adzatengedwa, ndipo onse adzada nalo nkhaŵa tsoka lao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Babiloni; ndi zimene walingirira dziko la Ababiloni; ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake imvani. Izi ndi zimene Ine Yehova ndakonza zolangira anthu a ku Babuloni. Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Babulo; ndi zimene walingirira dziko la Akasidi; ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.