Jeremiah 50:46 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko lonse lapansi lidzanjenjemera chifukwa cha kugwa kwa Babiloni. Kulira kwake kudzamveka pakati pa mitundu yonse ya anthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dziko lapansi linthunthumira, pa phokoso la kugwidwa kwa Babiloni, ndipo mfuu wamveka mwa amitundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akadzagwa Babuloni padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera, ndipo kulira kwawo kudzamveka pakati pa mitundu yonse ya anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dziko lapansi linthunthumira, pa phokoso la kugwidwa kwa Babulo, ndipo mpfuu wamveka mwa amitundu.