Jeremiah 50:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzafunsa njira ya ku Ziyoni, nkuyamba ulendo wobwerera kumeneko. Adzati, ‘Tiyeni tibwerere kwa Chauta, tikachite naye chipangano chamuyaya, chimene sichidzaiŵalika konse.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzafunsira Ziyoni nkhope zao zilikuyang'ana kumeneko, ndi kuti, Tiyeni inu, dzilumikizeni kwa Yehova m'chipangano cha muyaya chimene sichidzaiwalika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzafunsa njira ya ku Ziyoni ndi kuyamba ulendo wopita kumeneko. Iwo adzadzipereka kwa Yehova pochita naye pangano lamuyaya limene silidzayiwalika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzafunsira Ziyoni nkhope zao zirikuyang'ana kumeneko, ndi kuti, Tiyeni inu, dzilumikizeni kwa Yehova m'cipangano ca muyaya cimene sicidzaiwalika.