Jeremiah 50:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Anthu anga anali ngati nkhosa zotayika. Abusa ao adaŵasokeza ndi kuŵayalukitsa ku mapiri. Ankangoyendayenda ku zitunda ndi ku mapiri, mpaka kuiŵala kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu anga anakhala nkhosa zotayika; abusa ao anazisokeretsa pa mapiri onyenga; achoka kuphiri kunka kuchitunda; aiwala malo ao akupuma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu anga ali ngati nkhosa zotayika; abusa awo anawasocheretsa mʼmapiri. Iwo anayendayenda mʼmapiri ndi mʼzitunda mpaka kuyiwala kwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu anga anakhala nkhosa zotayika; abusa ao anazisokeretsa pa mapiri onyenga; acoka kuphiri kunka kucitunda; aiwala malo ao akupuma.