Jeremiah 50:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzasankha ndi kubwera nalo gulu lankhondo lamphamvu la mitundu ina ya anthu lochokera kumpoto, kuti lidzamenyane ndi Babiloni. Mivi yao ili ngati ya wankhondo waluso, yosapita padera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babiloni msonkhano wa mitundu yaikulu kuchokera kudziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babiloni adzachotsedwa; mivi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera chabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, ndidzaukitsa gulu lankhondo lamphamvu la mitundu ina ndi kubwera nalo kuchokera kumpoto kudzamenyana ndi Babuloni. Iwo adzandandalika ankhondo awo ndi kugonjetsa Babuloni. Mivi yawo ili ngati ya ankhondo aluso, yosapita padera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babulo msonkhano wa mitundu yaikuru kucokera ku dziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babulo adzacotsedwa; mibvi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera cabe.