Jeremiah 51:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Songolani mivi, tengani zishango.” Chauta wautsa mitima ya mafumu a Amedi, poti cholinga chake nchoti aononge Babiloni. Afuna kumlipsira chifukwa choononga Nyumba yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yehova wadzutsa mitima ya mafumu a Amedi, popeza cholinga chake ndi kuwononga Babuloni. Motero adzalipsira Ababuloni chifukwa chowononga Nyumba yake. Ndiye Yehova akuti, ‘Nolani mivi, tengani zishango.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nolani mibvi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; cifukwa alingalirira Babulo kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera cilango kwa Yehova; kubwezera cilango cifukwa ca Kacisi wace.