Jeremiah 51:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwezani mbendera yankhondo ndipo muwononge malinga a Babiloni. Mulimbitse oteteza, muike alonda, mukonzekere kulalira. Pakuti Chauta watsimikiza, ndipo adzachitadi zimene adanena za anthu a ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muwakwezere mbendera makoma a Babiloni, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kuchita chomwe ananena za okhala m'Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwezani mbendera yankhondo kuti muwononge malinga a Babuloni! Limbitsani oteteza, ikani alonda pa malo awo, konzekerani kulalira. Pakuti Yehova watsimikiza ndipo adzachitadi zomwe ananena za anthu a ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muwakwezere mbendera makoma a Babulo, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kucita comwe ananena za okhala m'Babulo.