Jeremiah 51:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse adalumbira pali Iye yemwe mwini wake kuti, “Ndidzatuma anthu osaŵerengeka ngati dzombe kuti adzakuthireni nkhondo, ndipo adzafuula, kuwonetsa kuti apambana.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wa makamu walumbira pa Iye mwini, kuti, Ndithu ndidzakudzaza iwe ndi anthu, monga ndi madzombe; ndipo adzakukwezera iwe mfuu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse analumbira pali Iye mwini kuti: Ndidzakutumizira adani ochuluka ngati dzombe, kuti adzakuthire nkhondo ndipo adzafuwula kuonetsa kuti apambana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wa makamu walumbira pa Iye mwini, kuti, Ndithu ndidzakudzaza iwe ndi anthu, monga ndi madzombe; ndipo adzakukwezera iwe mpfuu.