Jeremiah 51:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye akalankhula, kumamveka mkokomo wa madzi kumwamba, ndiye amene amadzetsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Amang'animitsa mphezi za mvula, amakunthitsa mphepo kuchokera kumene amaisunga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamene Iye anena mau, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, ayesa mphezi ya mvula, atulutsa mphepo ya m'nyumba za chuma zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba. Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvula ndi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene amasungira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamene Iye anena mau, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, ayesa mphezi ya mvula, aturutsa mphepo ya m'nyumba za cuma zace.