Jeremiah 51:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Mulungu wa Yakobe sali ngati mafanowo, Iye ndiyedi Mlengi wa zonse. Aisraele ndi anthu ake amene Iye adaŵasankha, dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndi mtundu wa cholowa chake, dzina lake ndi Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo. Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse, kuphatikizapo mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake. Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israyeli ndi mtundu wa colowa cace, dzina lace ndi Yehova wa makamu.