Jeremiah 51:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzatuma alendo ku Babiloni, kuti adzampepete ndi kuseseratu zonse zokhala m'dziko lake. Iwowo adzamuukira pa mbali zonse nthaŵi ya zoopsayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzatuma ku Babiloni alendo, amene adzampeta iye, amene adzataya zonse m'dziko lake, pakuti tsiku la chisauko adzamenyana ndi iye pomzungulira pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzatuma alendo ku Babuloni kudzamupeta ndi kuwononga dziko lake kotheratu. Iwo adzalimbana naye ku mbali zonse pa tsiku la masautso ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzatuma ku Babulo alendo, amene adzamkupira iye, amene adzataya zonse m'dziko lace, pakuti tsiku la cisauko adzamenyana ndi iye pomzungulira pace.