Jeremiah 51:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya amuna ndi akazi ao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya nkhalamba ndi achinyamata. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya anyamata ndi anamwali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi iwe ndidzathyolathyola galeta ndi iye wokweramo; ndi iwe ndidzathyolathyola mwamuna ndi mkazi; ndi iwe ndidzathyolathyola wokalamba ndi mnyamata; ndi iwe ndidzathyolathyola mnyamata ndi namwali;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi iwe ndimaphwanya mwamuna ndi mkazi, ndi iwe ndimaphwanya nkhalamba ndi wachinyamata, ndi iwe ndimaphwanya mnyamata ndi namwali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi iwe ndidzatyolatyola gareta ndi iye wokweramo; ndi iwe ndidzatyolatyola mwamuna ndi mkazi; ndi iwe ndidzatyolatyola wokalamba ndi mnyamata; ndi iwe ndidzatyolatyola mnyamata ndi namwali;