Jeremiah 51:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kwezani mbendera yankhondo pa dziko, lizani lipenga kuti mitundu ya anthu imve. Itanani mitundu yonse kuti imuthire nkhondo Babiloni. Itanani maufumu a ku Ararati, a ku Mini ndi a ku Asikenazi. Ikani mtsogoleri wankhondo kuti amenyane ndi Babiloniyo. Mubweretse akavalo ochuluka ngati dzombe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwezani mbendera m'dziko, ombani lipenga mwa amitundu, konzerani amitundu amenyane naye, mummemezere maufumu a Ararati, Mini, ndi Asikenazi; muike nduna; amenyane naye; mukweretse akavalo ngati dzombe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kwezani mbendera ya nkhondo mʼdziko! Lizani lipenga pakati pa mitundu ya anthu! Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti ikamuthire nkhondo; itanani maufumu awa: Ararati, Mini ndi Asikenazi kuti adzamuthire nkhondo. Ikani mtsogoleri wankhondo kuti amenyane naye; tumizani akavalo ochuluka ngati magulu a dzombe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwezani mbendera m'dziko, ombani lipenga mwa amitundu, konzerani amitundu amenyane naye, mummemezere maufumu a Ararati, Mini, ndi Asikenaza; muike nduna; amenyane naye; mukweretse akavalo ngati mandowa.