Jeremiah 51:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sonkhanitsani mitundu ya anthu kuti imuthire nkhondo. Muitane mafumu a ku Medi, pamodzi ndi abwanamkubwa ndi nduna zao, ndiponso ankhondo a m'maiko onse amene amaŵalamulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Konzerani amitundu amenyane ndi iye, mafumu a Amedi, akazembe ake, ndi ziwanga zake zonse, ndi dziko lonse la ufumu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Konzekeretsani mitundu ya anthu. Amenewa ndiwo mafumu a Amedi, abwanamkubwa awo, atsogoleri a ankhondo, ndiponso ankhondo a mayiko amene amawalamulira, kuti idzathire nkhondo Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Konzerani amitundu amenyane ndi iye, mafumu a Amedi, akazembe ace, ndi ziwanga zace zonse, ndi dziko lonse la ufumu wace.