Jeremiah 51:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko likunjenjemera, likuphiriphitha chifukwa cha kupweteka, chifukwa zimene Chauta adakonzera Babiloni zidzachitikadi, zakuti adzamsandutsa dziko lachipululu lopanda anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dziko linthunthumira ndi kuphwetekedwa, pakuti zimene Yehova analingalirira Babiloni zilipobe, zoti ayese dziko la Babiloni bwinja lopanda wokhalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko likunjenjemera ndi kunthunthumira, chifukwa zidzachitikadi zimene Yehova wakonzera Babuloni; kusakaza dziko la Babuloni kuti musapezeke wokhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dziko linthunthumira ndi kuphwetekedwa, pakuti zimene Yehova analingalirira Babulo ziripobe, zoti ayese dziko la Babulo bwinja lopanda wokhalamo.