Jeremiah 51:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Okoka uta musaŵalekerere, kapena onyadira chovala chao chankhondo. Anyamata ake musasiyeko ndi mmodzi yemwe. Ankhondo ake onse muŵaononge.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wauta asakoke uta wake, asadzikweze m'malaya ake achitsulo; musasiye anyamata ake; muononge ndithu khamu lake lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Okoka uta musawalekerere kapena wonyadira chovala chawo chankhondo. Musawasiye anyamata ake kuti akhale ndi moyo; koma muwononge ankhondo ake kotheratu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wauta asakoke uta wace, asadzikweze m'malaya ace acitsulo; musasiye anyamata ace; muononge ndithu khamu lace lonse.