Jeremiah 51:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankhondo a ku Babiloni aleka kuponya nkhondo, angokhala khale m'malinga ao. Mphamvu zao zatha, asanduka ngati akazi. Nyumba zake zatenthedwa, mipiringidzo ya zipata zake yathyoka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Olimba a ku Babiloni akana kumenyana, akhala m'malinga ao; mphamvu yao yalephera; akhala ngati akazi; nyumba zake zapsa ndi moto; akapichi ake athyoka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ankhondo a ku Babuloni aleka kuchita nkhondo; iwo angokhala mʼmalinga awo. Mphamvu zawo zatheratu; ndipo akhala ngati akazi. Malo ake wokhala atenthedwa; mipiringidzo ya zipata zake yathyoka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Olimba a ku Babulo akana kumenyana, akhala m'malinga ao; mphamvu yao yalephera; akhala ngati akazi; nyumba zace zapsya ndi moto; akapici ace atyoka.