Jeremiah 51:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Babiloni wokongola uja wangokhala ngati popunthira tirigu pa nthaŵi yopuntha kumene. Ndipotu posachedwa nthaŵi yake yokolola ifika,” akutero Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Mwana wamkazi wa Babiloni akunga dwale pamene aliunda; patsala kanthawi kakang'ono, ndipo nthawi yamasika idzamfikira iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Babuloni wokongola uja wakhala ngati malo opunthirapo tirigu pa nthawi yake yopuntha tirigu; A ku Yerusalemu akuti, Posachedwapa nthawi yake yomukolola ifika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Mwana wamkazi wa Babulo akunga dwale pamene aliunda; patsala kanthawi kakang'ono, ndipo nthawi yamasika idzamfikira iye.