Jeremiah 51:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
A ku Yerusalemu akuti, “Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, watiwononga, Watitswanya ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu. Watimeza ngati ng'ona. Wakhuta ndi zakudya zathu zotsekemera, kenaka nkutilavula.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng'ona, wadzaza m'kamwa mwake ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
A ku Yerusalemu akuti, “Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni watiwononga, watiphwanya, ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu. Watimeza ngati ngʼona, wakhuta ndi zakudya zathu zokoma, kenaka nʼkutilavula.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng'ona, wadzaza m'kamwa mwace ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine,