Jeremiah 51:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu okhala m'Ziyoni anene kuti, “Zankhanza zimene Ababiloni adatichita ife ndi ana athu ziŵabwerere.” Anthu okhala mu Yerusalemu anene kuti, “Magazi athu amene adamwazika aŵagwere Ababiloniwo ngati chilango chao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wokhala m'Ziyoni adzati, Chiwawa anandichitira ine ndi thupi langa chikhale pa Babiloni; nadzati Yerusalemu, Mwazi wanga ukhale pa okhala m'Kasidi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Ziyoni anene kuti, “Zankhanza zimene anatichitira ife ziwabwerere Ababuloni.” Anthu okhala mu Yerusalemu anene kuti, “Magazi athu amene anakhetsedwa akhale pa amene akukhala ku Babuloni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wokhala m'Ziyoni adzati, Ciwawa anandicitira ine ndi thupi langa cikhale pa Babulo; nadzati Yerusalemu, Mwazi wanga ukhale pa okhala m'Kasidi.