Jeremiah 51:39 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akachita dyera, ndidzaŵakonzera madyerero. Tsono ndidzaŵaledzeretsa, ndipo adzasangalala nkugona tulo tampakampaka, osadzukanso ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene atentha, ndidzakonza madyerero ao, ndidzawaledzeretsa, kuti asangalale, agone chigonere, asanyamuke, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati achita dyera ndiye ndidzawakonzera madyerero ndi kuwaledzeretsa, kotero kuti adzasangalala, kenaka nʼkugona tulo mpaka muyaya ndipo sadzadzukanso,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene atentha, ndidzakonza madyerero ao, ndidzawaledzeretsa, kuti asangalale, agone cigonere, asanyamuke, ati Yehova.