Jeremiah 51:43 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mizinda yake yasanduka malo onyansa, dziko louma ndi lachipululu, dziko lopanda anthu losayendako mwanawamunthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Midzi yake yakhala bwinja, dziko louma, chipululu mosakhalamo anthu, mosapita mwana wa munthu aliyense.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mizinda yake yasanduka bwinja, dziko lowuma ndi lachipululu, dziko losakhalamo wina aliyense, dziko losayendamo munthu aliyense.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Midzi yace yakhala bwinja, dziko louma, cipululu mosakhalamo anthu, mosapita mwana wa munthu ali yense.