Jeremiah 51:47 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono ikudza nthaŵi pamene ndidzalange mafano a Babiloni. Dziko lonselo lidzachita manyazi. Anthu ake onse ophedwa adzakhala ali ngundangunda pakati pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, amene ndidzaweruza mafano osemasema a Babiloni, ndipo dziko lake lonse lidzakhala ndi manyazi; ndipo ophedwa ake onse adzagwa pakati pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti taonani, nthawi ikubwera ndithu pamene ndidzalanga mafano a ku Babuloni; dziko lake lonse lidzachita manyazi ndi ophedwa ake onse adzakhala ngundangunda pakati pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, taonani, masiku alinkudza, amene ndidzaweruza mafano osemasema a Babulo, ndipo dziko lace lonse lidzakhala ndi manyazi; ndipo ophedwa ace onse adzagwa pakati pace.