Jeremiah 51:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Israele ndi Yuda sadasiyidwe ndi Mulungu wao, Chauta Wamphamvuzonse. Koma dziko la Ababiloni nlodzaza ndi machimo, machimo ake onyoza Woyera uja wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Israele ndi Yuda sasiyidwa ndi Mulungu wao, ndiye Yehova wa makamu: ngakhale dziko lao ladzala ndi uchimo kuchimwira Woyera wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Yuda ndi Israeli sanasiyidwe ngati amasiye ndi Mulungu wawo, Yehova Wamphamvuzonse, koma ngakhale dziko la Babuloni ndi lodzaza ndi machimo pamaso pa Woyerayo wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Israyeli ndi Yuda sasiyidwa ndi Mulungu wao, ndiye Yehova wa makamu: ngakhale dziko lao ladzala ndi ucimo kucimwira Woyera wa Israyeli.