Jeremiah 51:53 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale Babiloni adzikweze mpaka ku mlengalenga, nkulimbitsa nsanja zake, ndidzatuma oononga kuti amgonjetse,” akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngakhale Babiloni adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yake, koma kuchokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale Babuloni atadzikweza mpaka mlengalenga ndi kulimbitsa nsanja zake, ndidzatuma anthu owononga kudzamenyana naye,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngakhale Babulo adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yace, koma kucokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova.