Jeremiah 51:56 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Woononga amufikira Babiloni, ndipo ankhondo ake onse agwidwa, mauta ao athyoka. Pajatu Chauta ndi Mulungu wolanga, adzabwezeradi kwathunthu zoipa zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti wakufunkha wafika kwa iye, kwa Babiloni, ndi anthu ake olimba agwidwa, mauta ao athyokathyoka, pakuti Yehova ndiye Mulungu wakubwezera, adzabwezera ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti wowononga wafika kudzamenyana ndi Babuloni, ankhondo ake agwidwa, ndipo mauta awo athyoka. Paja Yehova ndi Mulungu wobwezera chilango; adzabwezera kwathunthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti wakufunkha wafika kwa iye, kwa Babulo, ndi anthu ace olimba agwidwa, mauta ao atyokatyoka, pakuti Yehova ndiye Mulungu wakubwezera, adzabwezera ndithu.