Jeremiah 51:58 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Malinga aakulu a Babiloni adzasalazidwa. Zipata zake zazitali zidzatenthedwa. Mitundu ya anthu idagwira ntchito pachabe, anthu adangotopa nkumanga zimene tsopano zikupsa ndi moto.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wa makamu atero: Makoma otakata a Babiloni adzagwetsedwa ndithu, ndi zitseko zake zazitali zidzatenthedwa ndi moto; anthu adzagwirira ntchito chabe, ndi mitundu ya anthu idzagwirira moto, nidzatopa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Malinga aakulu a Babuloni adzasalazidwa ndipo zipata zake zazitali zidzatenthedwa; mitundu ya anthu inangogwira ntchito pachabe. Anthu anatopa ndi kumanga zimene tsopano zikupsa ndi moto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wa makamu atero: Makoma otakata a Babulo adzagwetsedwa ndithu, ndi zitseko zace zazitari zidzatenthedwa ndi moto; anthu adzagwirira nchito cabe, ndi mitundu ya anthu idzagwirira moto, nidzatopa.