Jeremiah 51:59 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Zedekiya anali ndi phungu wake wamkulu, dzina lake Seraya, mwana wa Neriya, mdzukulu wa Maseiya. Pa chaka chachinai cha ufumu wa Zedekiya ku Yuda, Seraya adatsagana ndi mfumuyo kupita ku Babiloni. Tsono mneneri Yeremiya adampatsirako uthenga Serayayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mau amene Yeremiya mneneri anauza Seraya mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamene iye ananka ndi Zedekiya mfumu ya Yuda ku Babiloni chaka chachinai cha ufumu wake. Ndipo Seraya anali kapitao wa chigono chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zedekiya mfumu ya Yuda inali ndi phungu wake wamkulu amene dzina lake linali Seraya mwana wa Neriya chidzukulu cha Maseya. Mʼchaka chachinayi cha ulamuliro wake, Zedekiya anapita ndi Seraya ku Babuloni. Tsono mneneri Yeremiya anamupatsirako uthenga Serayayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mau amene Yeremiya mneneri anauza Seraya mwana wa Neriya, mwana wa Maseya, pamene iye ananka ndi Zedekiya mfumu ya Yuda ku Babulo caka cacinai ca ufumu wace. Ndipo Seraya anali kapitao wa cigono cace.