Jeremiah 51:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Aliyense mwa inu athaŵe, achoke ku Babiloni kuti apulumutse moyo wake. Musaphedwe naye pamodzi pamene adzalandira chilango chake. Limeneli ndilodi tsiku limene Chauta adzaŵalanga, ndipo adzaŵalipsira kwathunthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Thawani pakati pa Babiloni, yense apulumuke moyo wake; musathedwe m'choipa chake; pakuti ndi nthawi ya kubwezera chilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Thawaniko ku Babuloni! Aliyense apulumutse moyo wake! Musawonongeke naye pamodzi chifukwa cha machimo ake. Imeneyi ndi nthawi yoti Yehova amulange; Yehova adzamulipsira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Thawani pakati pa Babulo, yense apulumuke moyo wace; musathedwe m'coipa cace; pakuti ndi nthawi ya kubwezera cilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yace.