Jeremiah 51:64 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ukanene kuti, ‘Umu ndimo m'mene Babiloni adzamirire. Sadzadzukanso chifukwa cha zoopsa zonse zimene ndidzamgwetsere.’ ” Mau a Yeremiya athera pamenepa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nuti, Chomwecho adzamira Babiloni, sadzaukanso chifukwa cha choipa chimene ndidzamtengera iye; ndipo adzatopa. Mau a Yeremiya ndi omwewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ukanene kuti, ‘Umu ndi mmene adzamirire Babuloni ndipo sadzadzukanso chifukwa cha masautso amene adzamugwere.’ ” Mawu a Yeremiya athera pamenepa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nuti, Comweco adzamira Babulo, sadzaukanso cifukwa ca coipa cimene ndidzamtengera iye; ndipo adzatopa. Mau a Yeremiya ndi omwewo.