Jeremiah 51:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu Babiloni anali ngati chikho chagolide m'manja mwa Chauta, kuti aledzeretse dziko lonse lapansi. Mitundu yambiri ya anthu idamwako vinyo wake, nchifukwa chake idapenga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Babiloni wakhala chikho chagolide m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wake; chifukwa chake amitundu ali ndi misala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Babuloni anali ngati chikho cha golide mʼdzanja la Yehova; kuti aledzeretse dziko lonse lapansi. Mitundu yambiri ya anthu inamwa vinyo wake; nʼchifukwa chake tsopano inachita misala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Babulo wakhala cikho cagolidi m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wace; cifukwa cace amitundu ali ndi misala.