Jeremiah 51:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ena adati, ‘Tidayesa kumpatsa mankhwala koma sadachire. Tiyeni tingomsiya, timchokere ndipo aliyense apite ku dziko lakwao. Paja mlandu wake wafika mpaka kumwamba, wafika mpaka ku mlengalenga.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tikadachiritsa Babiloni koma sanachire; mumsiye iye, tipite tonse yense kudziko lake; pakuti chiweruziro chake chifikira kumwamba, chinyamulidwa mpaka kuthambo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena anati, “ ‘Ife tinayesa kumupatsa mankhwala Babuloni, koma sanachire; tiyeni timusiye ndipo aliyense apite ku dziko la kwawo, pakuti mlandu wake wafika mpaka mlengalenga, wafika mpaka kumwamba.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tikadaciritsa Babulo koma sanacire; mumsiye iye, tipite tonse yense ku dziko lace; pakuti ciweruziro cace cifikira kumwamba, cinyamulidwa mpaka kuthambo,