Jeremiah 52:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zedekiya anali wa zaka 21 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Hamutala, mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zedekiya anali wa zaka makumi awiri kudza chimodzi pamene analowa ufumu wake; ndipo analamulira m'Yerusalemu zaka khumi kudza chimodzi; dzina la amake ndi Hamutala mwana wamkazi wa Yeremiya wa ku Libina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zedekiya anali wa zaka 21 pamene analowa ufumu, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Amayi ake anali Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zedekiya anali wa zaka makumi awiri kudza cimodzi pamene analowa ufumu wace; ndipo analamulira m'Yerusalemu zaka khumi kudza cimodzi; dzina la amace ndi Hamutala mwana wamkazi wa Yeremiya wa ku Libina.