Jeremiah 52:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pompo adapha ana a Zedekiya iyeyo akupenya. Adaphanso akalonga onse a ku Yuda ku Ribula komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya ku Babiloni inapha ana a Zedekiya pamaso pake; niphanso akulu onse a Yuda m'Ribula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ku Ribulako mfumu ya ku Babuloni inapha ana aamuna a Zedekiya iyeyo akuona; ndiponso inapha akuluakulu onse a ku Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya ku Babulo inapha ana a Zedekiya pamaso pace; niphanso akuru onse a Yuda m'Ribila.