Jeremiah 52:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwezi wachisanu, pa tsiku lakhumi la mwezi, chaka cha 19 cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, mmodzi wa aphungu ake, adadza ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, ndicho chaka chakhumi ndi chisanu ndi chinai cha Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, analowa m'Yerusalemu Nebuzaradani kapitao wa alonda, amene anaimirira pamaso pa mfumu ya ku Babiloni:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwezi wachisanu, pa tsiku lakhumi, chaka cha 19 cha ulamuliro wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo a mfumu, amene amatumikira mfumu ya ku Babuloni, anabwera ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwezi wacisanu, tsiku lakhumi la mwezi, ndico caka cakhumi ndi cisanu ndi cinai ca Nebukadirezara, mfumu ya ku Babulo, analowa m'Yerusalemu Nebuzaradani kapitao wa alonda, amene anaimirira pamaso pa mfumu ya ku Babulo: