Jeremiah 52:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena onse amene adaatsala mumzindamo, ndi ena amene adaadzipereka kale kwa mfumu ya ku Babiloni, pamodzi ndi anthu aluso otsala, Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja adaŵatenga kupita nawo ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende anthu aumphawi, ndi anthu otsala amene anatsala m'mudzi, ndi amene anapandukira, kutsata mfumu ya ku Babiloni, ndi otsala a unyinjiwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, anthu aluso pamodzi ndi amene anadzipereka kale kwa mfumu ya ku Babuloni kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende anthu aumphawi, ndi anthu otsala amene anatsala m'mudzi, ndi amene anapandukira, kutsata mfumu ya ku Babulo, ndi otsala a unyinjiwo.