Jeremiah 52:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Nebuzaradani adasiyako anthu ena osauka kwambiri am'dzikomo, kuti azilima minda ya mphesa ndi minda ina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya aumphawi a padziko akhale akulima mphesa ndi akulima m'minda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo anasiya anthu ena onse osaukitsitsa a mʼdzikomo kuti azigwira ntchito mʼminda ya mpesa ndi minda ina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya aumphawi a padziko akhale akulima mphesa ndi akulima m'minda.