Jeremiah 52:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankhondo a ku Babiloni adaphwanya nsanamira zamkuŵa za m'Nyumba ya Chauta, ndiponso maphaka ndi chimbiya chamkuŵa, ndipo adatenga mkuŵa wonsewo, napita nawo ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mizati yamkuwa imene inali m'nyumba ya Yehova, ndi zoikapo ndi thawale lamkuwa zimene zinali m'nyumba ya Yehova, Ababiloni anazithyolathyola, nanka nao mkuwa wake wonse ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ababuloni anaphwanya nsanamira za mkuwa, maphaka ndi chimbiya chamkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova. Anatenga mkuwa wonsewo nʼkupita nazo ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mizati yamkuwa imene inali m'nyumba ya Yehova, ndi zoikapo ndi thawale lamkuwa zimene zinali m'nyumba ya Yehova, Akasidi anazityolatyola, nanka nao mkuwa wace wonse ku Babulo.