Jeremiah 52:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nsanamira imodzi kutalika kwake inali mamita asanu ndi atatu, kuzungulira kwake inali mamita asanu ndi theka. Inali ndi chiboo m'kati, ndipo kuchindikira kwake inali zala zinai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma nsanamirazo, utali wake wa nsanamira ina unafikira mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndi chingwe cha mikono khumi ndi iwiri chinaizinga; kuchindikira kwake kunali zala zinai; inali yagweregwere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nsanamira imodzi kutalika kwake kunali mamita asanu ndi atatu, akazunguliza chingwe inali mamita asanu ndi theka; mʼkati mwake munali bowo ndipo kuchindikala kwake kunali zala zinayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma nsanamirazo, utari wace wa nsanamira yina unafikira mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndi cingwe ca mikono khumi ndi iwiri cinaizinga; kucindikira kwace kunali zala zinai; inali yagweregwere.