Jeremiah 52:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inali ndi mutu wamkuŵa, kutalika kwake mamita aŵiri. Pozungulira mutuwo panali ukonde ndi makangaza, zonsezo zamkuŵa. Nsanamira inayo inalinso ndi makangaza ndipo inkafanana ndi inzakeyo pa zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo korona wamkuwa anali pamwamba pake; utali wake wa korona mmodzi unali wa mikono isanu, ndi sefa ndi makangaza pakorona pozungulira pake, onse amkuwa: nsanamira inzake yomwe inali nazo zonga zomwezi, ndi makangaza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamwamba pa nsanamira iliyonse panali mutu wamkuwa umene kutalika kwake kunali mamita awiri. Pozungulira pake panali ukonde ndi makangadza, zonsezo za mkuwa. Nsanamira inayo inalinso ndi makangadza ake ndipo inali yofanana ndi inzake ija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo korona wamkuwa anali pamwamba pace; utari wace wa korona mmodzi unali wa mikono isanu, ndi made ndi makangaza pakorona pozungulira pace, onse amkuwa: nsanamira inzace yomwe inali nazo zonga zomwezi, ndi makangaza.