Jeremiah 52:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumzindamo adagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo, ndiponso anthu asanu ndi aŵiri amene anali aphungu a mfumu mumzindamo. Adagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo, amene ankalemba anthu am'dzikomo, ndiponso akuluakulu ena 60, amene anali mumzindamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo m'mudzi anatenga kazembe amene anali woyang'anira anthu a nkhondo ndi amuna asanu ndi awiri a iwo akuona nkhope ya mfumu, amene anapezedwa m'mudzi; ndi mlembi wa kazembe wa nkhondo, amene akamemeza anthu a m'dziko; ndi amuna makamu asanu ndi limodzi a anthu a m'dziko, amene anapezedwa pakati pa mudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mu mzindamo anagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo, ndi alangizi amfumu asanu ndi awiri. Anagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo, amene ankalemba anthu mʼdzikomo, pamodzi ndi anthu ena 60 amene anali mu mzindamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo m'mudzi anatenga kazembe amene anali woyang'anira anthu a nkhondo ndi amuna asanu ndi awiri a iwo akuona nkhope ya mfumu, amene anapezedwa m'mudzi; ndi mlembi wa kazembe wa nkhondo, amene akamemeza anthu a m'dziko; ndi amuna makumi asanu ndi limodzi a anthu a m'dziko, amene anapezedwa pakati pa mudzi.