Jeremiah 52:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ya ku Babiloni idalamula kuti onsewo aphedwe ku Ribula m'dziko la Hamati. Motero anthu a ku Yuda adatengedwa ukapolo kuŵachotsa kutali ndi dziko lao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya ku Babiloni anawakantha, nawapha pa Ribula m'dziko la Hamati. Chomwecho Yuda anatengedwa ndende kutuluka m'dziko lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ku Ribulako, mʼdziko la Hamati, mfumu ya ku Babuloniyo inalamula kuti anthuwo aphedwe. Motero anthu a ku Yuda anapita ku ukapolo, kutali ndi dziko lawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya ku Babulo anawakantha, nawapha pa Ribila m'dziko la Hamati. Comweco Yuda anatengedwa ndende kuturuka m'dziko lace.