Jeremiah 52:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa cha zonse zimene zidachitika ku Yerusalemu ndi ku Yudazi, Chauta adakwiya kwambiri, mpaka kuŵachotsa anthuwo pamaso pake. Tsono Zedekiya adapandukira mfumu ya ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti zonse zinachitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda chifukwa cha mkwiyo wa Yehova, mpaka anawachotsa pamaso pake; ndipo Zedekiya anampandukira mfumu ya Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha zonse zimene zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda Yehova anakwiyira anthu ake mpaka kuwachotsa pamaso pake. Tsono Zedekiya anawukira mfumu ya ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti zonse zinacitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda cifukwa ca mkwiyo wa Yehova, mpaka anawacotsa pamaso pace; ndipo Zedekiya anampandukira mfumu ya Babulo.